ebook img

Mtanthauziramawu wa Chinyanja PDF

648 Pages·2.859 MB·Published by the Centre for Language Studies
Save to my drive
Quick download
Download
Most books are stored in the elastic cloud where traffic is expensive. For this reason, we have a limit on daily download.

Preview Mtanthauziramawu wa Chinyanja

Mtanthauziramawu wa Chinyanja Published by the Centre for Language Studies A A, a1 /k/ dzi. Mu-A- (zambi. ma a) lembo loyamba mu mndandanda wa malembo a m’chiyankhulo cha Chichewa ndiponso limodzi la malembo asanu aliwu: a, e, i, o, u. a2 dzi. Mu-A- (zambi. ma a) mawu osonyeza ulemu potchula dzina la munthu. lero kuli mowa kwa a Chintengo aa1 /k/ mfu. mawu osonyeza kudabwa, kutsutsa, kapena kusakondwa ndi zochitika. aa! zatero? aa! ine sindinali nawo aa2 /k/ mfu. mawu onena poinga nkhuku, mbalame ndi zina. anafuula kuti ‘aa! aa!’ kuinga nkhuku zomwe zinali kujompha ufa. abakadya /ttkt/ dzi. Mu-A (zambi. abakadya) chilonda chosapola mpaka imfa kapena chilonda chamgonagona. anayesa kuthira mankhwala osiyanasiyana pa chilondacho kuti chipole koma chifukwa chosachisamalira bwino chinasanduka abakadya abee /tk/ mfu. mawu amene akazi amanena povomera kuitanidwa. pamene Maliya adamuyitana amake adavomera kuti ‘abee’ abwito /tkt/ dzi. Mu-A- (zambi. abwito) tinthu tonga mafinya totuluka m’maso chakumphepete (manthongo). nditadzuka m’mawa, ndinapita kukasukusula kumaso pofuna kuchotsa abwito achale (Nge) /kt/ Mu-A- (zambi. achale) chakudya chokometsera ndiwo chopangidwa posakaniza tsabola wambiri ndi zipatso monga mango, anyezi ndi adyo. amwenye ambiri amakonda kudya zakudya zatsabola wambiri monga achale adakulasa dzi. Mu-A- (zambi. adakulasa) kagulu ka nyenyezi zisanu ndi ziwiri zowala bwino. mae.: msangwe, akamwiniatsatana, mauta. atayang’ana kumwamba, adachita chidwi ndi kagulu ka nyenyezi kowala kwambiri ndipo agogo ake adamuwuza nyenyezi zotero amazitcha adakulasa adiresi (Nge) dzi. I-zi- (zambi. adiresi) dzina la malo amene munthu amakhala. mae.: keyala. ndimati mundipatse adiresi yanu kuti ndidzakulembereni kalata ndikadzafika kumudzi. adyo /kt/ Mu-A- (zambi. adyo) mtundu wa chomera chokhala ndi thima loyerera ndi masamba obiriwira motuwira chafungo lamphamvu chomwe anthu amakometsera chakudya makamaka ndiwo. fani: anyezi. pitani kumsika kukagula adyo kuti tidzathire ndiwo aironi (Nge) /kt/ dzi. I-Zi- (zambi. aironi) chipangizo chomwe amayikamo moto wamakala kapena wamagetsi ndi kumasitira zovala. mae.: simbi. a Phiri anayika moto wamakala mu aironi kuti asite zovala zawo. akamwiniatsatana /tkkkt/ dzi. Mu-A- (zambi. akamwiniatsatana) onani tanthauzo la adakulasa akutsano1 /tk/ dzi. Mu-A- (zambi. akutsano) 1 amake a mfumu. a Nasimango monga akutsano obereka mfumu Chinkombero analandira ulemu woposa pa mwambo wolonga mfumuyi 2 mkazi wa mfumu. a Namulauzi, omwe tsopano akwatiwa ndi mfumu, anawalangiza kuti iwo monga akutsano ayenera kukhala munthu woyanjanitsa anzawo. akwaa /tk/ mfu. mawu osonyeza kudabwa, kukhumudwa ndi zochitika. mae.: ekwee, asaa, alaa. akwaa! monga mwana uja wamwaliradi. alaa /tk/ mfu. onani tanthauzo la akwaa. aleluya (Heb) /ttkt/ mfu. aleluya ndi mawu otanthawuza ‘lemekezani Yehova. ’. tikondwere! pamene mwana anapulumuka pa ngozi yowopsayo, tonse tinafuula mwachimwemwe kuti ‘aleluya!’ Allah (Arab) /kt/ dzi. Mu-A- . Allah ndi mawu omwe anthu achipembedzo chachisilamu amatchulira Mulungu. pamene anasonkhana ku msikiti, asilamu anathokoza Allah chifukwa cha zabwino zomwe amawachitira. alumali /ttkt/ dzi. Mu-A- (zambi. alumali) tsanja loyikapo zinthu makamaka zogulitsa m’sitolo kapena m’golosale. a Phiri anagula katundu wa m’sitolo mwawo ndipo anamusanja pa alumali kuti makasitomala awo azitha kumuwona bwino. alungu dzi. Mu-A- (zambi. alungu) 1 mizimu ya anthu akufa. mae.: amanda. 2 maloto kapena masomphenya momwe anthu amaona anthu akufa. usiku ndalota alungu akundiwuza uti ana amasiyewa tiziwasamala ngati athu omwe amanda1 Mu-A- (zambi. amanda) onani tanthauzo 1 la alungu amanda2 dzi. Mu-A- (zambi. amanda) mtundu wa mpunga womwe umakhala wonunkhira kwambiri. alimi ambiri a kudera la nyanja ya Chirwa amakonda kubzala mpunga wa amanda. ambulasi (Nge) dzi. (zambi. ambulasi) galimoto lomwe limakhala ndi zipangizo zapadera lomwe limatenga munthu wodwala kapena wovulala kupita naye ku chipatala. matenda atakula, dokotala wa pachipatala chaching’ono anayitanitsa ambulasi kuti itenge wodwalayo kupita naye kuchipatala chachikulu. ambulera (Nge) /tkkt/ dzi. I-Zi- (zambi. ambulera) ambulera ndi chinthu chopangidwa ndi nsalu yoterera yokungidwa ndi chokhala ndi chigwiriro chomwe anthu amafunda podziteteza ku mvula kapena dzuwa. dzulo kunali mvula yambiri ndipo ndinanyowa chifukwa ndinalibe ambulera ambwana (Sho) /kt/ dzi. Mu-A- (zambi. ambwana) mawu oyitanira anthu olingana msinkhu kutanthauza mnzanga. mae.: ayise, bwanawe, mwaiwe. ambwana, tiye tizipita kunyumba popeza kunjaku kwada. ame (Heb) mfu. mawu omwe akhirisitu amanena potsiriza pemphero kapena nyimbo kutanthauza kuti ‘kukhale choncho. ’. atatsiriza pemphero lopempherera wogwalayo, onse anayankha kuti ‘ame. ’. andiroko (Afr) /kt/ dzi. Mu-A- (zambi. andiroko) chovala cham’kati chonga siketi chomwe amavala akazi. andiroko ya Nabiyeni yabooka choncho wapita kwa telala kukasoketsa. . anyezi (Nge) /kt/ dzi. Mu-A- (zambi. anyezi) mtundu wa chomera chonga adyo chafungo la mphamvu koma losiyana ndi la adyo, chokometsera chakudya makamaka ndiwo. pitani kumsika mukagule anyezi kuti tidzathire ndiwo. apiro (Nge) dzi. I-Zi- pempho limene munthu amapereka kwa mkulu woweruza milandu kuti mlandu wake wa munthu wopemphayo ukaweruzidwe ku khoti lina lapamwamba chifukwa chosakhutira ndi momwe khoti loyambalo laweruzira mlanduwo. khoti linagamula kuti mlondayo amangidwe zaka zisanu chifukwa chopezeka ndi mlandu wakuba koma iye sanakhutitsidwe ndi chigamulochi choncho anachita apiro ku khoti lalikulu. asa /tk/ mfu. onani tanthauzo la akwaa. asa! bwanji mukuchita phokoso pamene anzanu akuwerenga? asi /tk/ muo. mawu osonyeza kukana. kunekwi.: ashi. mae.: ayi. asi, sindipita kuphwando la ukwati popeza ndikudwala. asikolo /kt/ (Nge) I-Zi- (zambi. asikolo) chitsulo kapena thabwa loikamo magalasi lomwe amamangirira ku feremu la zenera. kunekwi.: atikolo. pamene amamanga nyumba anayika asikolo ya magalasi asanu ndi limodzi pa zenera la chipinda cha ana. atulo /ttk/ dzi. Mu-A- (zambi. atulo) maganizo odza mwa munthu pamene ali mtulo ndipo zinthu za m’maganizozo zimakhala ngati zoona. mae.: maloto. usiku wathawu amayi akhalira kubwebweta, atulo awavuta kwambiri. ayata /tkt/ dzi. Mu-A- (zambi. ayata) mphini zomwe akazi amatema m’matako ndi m’ntchafu. chinali chizolowezi cha akazi akale kutema mphini za ayata m’ntchafu ndi m’matako. ayi /tk/ muo. onani tanthauzo la asi. ayi, sindipita kuphwando la ukwati popeza ndikudwala. ayise /ttk/ dzi. (Nge) onani tanthauzo la ambwana. ayise, tiye tizipita kunyumba popeza kunjaku kwada. ayisikirimu (Nge) /kkt/ dzi. Mu-A- (zambi. ayisikirimu) chakudya chozuna chopanga posakaniza shuga, mkaka ndi zinthu zina za ufa monga kasitadi. ana ambiri amakonda kudya zakudya zotsekemera monga ayisikirimu. ayo /kt/ mfu. mawu osonyeza kudandaula chifukwa cha chisoni kapena kupweteka kwa m’thupi. mae.: koto!, mayo! anali kubuula kuti ‘ayo!’, ‘ayo!’ pamene thupi linali kuwaphwanya. B B, b dzi. Mu-A- (zambi. ma b) lembo lachiwiri mu mndandanda wa malembo a chiyankhulo cha Chichewa ndipo ndi limodzi mwa malembo opanda liwu khumi, mphambu zisanu ndi zinayi ba1 /k/ mve. 1 ‘ba’ ndi umo limamvekera phokoso la khasu pokumba pansi pouma kapena phokoso la chitseko potseka mwamphamvu. anamenyetsa chitseko kuti ba panthawi imene anali kuthamangitsa mbala 2 ‘ba’ ndi momwe chimaonekera chinthu chikamatulukira pabwalo kapena pakhomo mwadzidzidzi. antchito onse anadzidzimuka bwana atangoti ba mmawa kwambiri pa ofesipo. ba2 Ku-, mne. tenga chinthu cha mwini chomwe sichili chako mozembetsa. mae. : njonja, psasa. baa /tk/ mfu. mawu amene amamveka ng’ombe ikamalira. pamene ng’ombeyo inabayidwa pakhosi inalira kuti ‘baa!’. baba1 /kt/ dzi. Mu-A- (zambi. ababa) 1 dzina limene mwana amayitanira atate ake. baba, ndimapempha kuti mukandigulire malaya. 2 dzina loitanira munthu aliyense wamkulu, wamwamuna. kodi mwaswera bwanji baba? baba2 Ku-, mne. funa kumwa madzi kapena zinthu zina zamadzimadzi. atayenda ulendo wautali padzuwa anamva kubaba choncho anapempha madzi kuti amwe. babada Ku-, mne. menya pamutu kapena pafupa ndi chinthu monga ndodo. kunekwi.: boboda. mae.: babadula. aphunzitsi anababada pamutu ophunzira onse ochita phokoso. babadira Ku-, mne. New entry. seems to have the same meaning as badira below. babaika /tttk/ Ku-, mne. kayika pochita chinthu. chifukwa choti anali kubabaika pogula katunduyo, munthu wina wachangu anagula katundu yenseyo kuwasiya iwo akudandaula. babaiza Ku-, mne. phimba chinthu china pa chovala chosakwanira kapena choperewera. siketi yomwe anavala inali yayifupi choncho anababaiza ndi chitenje. babakula Ku-, mne. lowetsa mimba m’kati pakanthawi pokokera mpweya mkati. mae.: bakhula, befula, defula, fenkhula, nenkhula, kalima. consider: tamula mimba pakanthawi pokokera mpweya mkati. munthu wodwala chibayo amavutika kubabakula popeza m’thiti mwake mumapweteka. babanyira Ku-, mne. onani tanthauzo la babadira. bada muo. khala wopanda zovala m’thupi. mae.: buno, maliseche, mbulanda, psata, popeza anali ndi malaya amodzi komanso kabudula mmodzi ndiye akachapa amangokhala bada osavala kanthu. bade dzi. Li-Ma- (zambi. mabade) fupa la mutu lomwe limatchinjiriza bongo. kunekwi.: chibade. mae.: dambe, nkhadzi, nkhatho, chibada, chigadza. munthu wokwera mthuthuthu amavala chisoti choteteza bade la mutu wake pa ngozi. badira Ku-, mne. konza mtanda wa nsima m’sengwa kapena m’mbale ndi chipande kuti uoneke wosalala. mae.: babanyira. badwa Ku-, mne. tuluka m’mimba mwamayi pachiyambi cha moyo. kodi mwana wanu anabadwa chaka chanji? badza dzi. Li-Ma- (zambi. mabadza) chikho kapena chinthu chilichonse champhako monga bango chomaeta nemba mbali imodzi m’kumaimba povina gule wamganda kapena malipenga. povina gule wamalipenga anthu amayimba chipangizo chotchedwa badza. bafa (Nge) dzi. I-Zi-/ Li-Ma- (zambi. bafa/mabafa) 1 malo osambiramo. agogo anagwa kubafa pamene anali kusamba. 2 chiwiya chosambiramo. madziwo akafunda muwakhutulire mu bafa. bafuta /tkt/ dzi. I-Zi- (zambi. bafuta) mtundu wa nsalu yoyera,. yolimba koma yofewa ndiponso yoterera ngati mafuta. panthawi yolongedwa ufumu, amwale anavala mkanjo wa nsalu yabafuta. baibulo (Nge) /kt/ dzi. I-Zi-/ Li-Ma- (zambi. baibulo/mabaibulo) Bukhu Lopatulika la mawu a Mulungu. iwo amakonda kuwerenga baibulo tsiku lililonse madzulo asanagone. baji (Nge) dzi. I-Zi-/Li-Ma- (zambi. baji/mabaji) chizindikiro chachinthu chilichonse choika pachovala monga pa jekete kapena malaya. iye amakonda kuvala baji ya chipani chake posonyeza kuchinyadira. bakha Mu-A- (zambi. abakha) mbalame yoweta yonga tsekwe yokonda kusambira m’madzi ndipo mapazi ake ndi olukanalukana. bambo wanga amakonda kudya nyama yabakha bakha dzi. Mu-A- (zambi. abakha) mbalame yoweta yonga tsekwe yokonda kusambira m’madzi ndipo mapadzi ake ndi olukanalukana. bambo anga anapha bakha wonona dzulo. bakhalibakhali mve. umo amaonekera munthu kapena chinthu chikamachita chinthu mofulumira ndi mwaliwiro. anthu amachita bakhalibakhali nthawi yakummawa kuthamangira kuntchito zawo zosiyanasiyana. bakhula Ku-, mne. onani tanthauzo la babakula. munthu wodwala chibayo amavutika kubabakhula popeza m’thiti mwake mumapweteka. bala1 Ku-, mne. 1 tulutsa mwana kuchoka m’mimba monga amachitira munthu kapena nyama yaikazi. mbuzi yanga ija yabala mwana wakufa. 2 khala ndi zipatso monga imachitira mitengo. mae. : patsa. mtengo waukulu uja wabala mango ambiri chaka chino. 3 chita mabulu kapena undana monga umachitira ufa m’madzi ogaduka pokandira nsima. pepani nsimayi ili ndi mabulu popeza phala linabala panthawi yokandira. bala2 /kt/ dzi. Li-Ma- (zambi. mabala) malo amene atemedwa pakhungu mwatsopano apa. anali ndi bala pamwendo chifukwa galu anamuluma. bala3 (Nge) /kt/ dzi. Li-Ma- (zambi. mabala) malo ogulitsira ndi kumwerako mowa. amalume anali ndi matsire choncho anapita kubala kuti akamwe mowa. balala /k/ mve. umo zimaonekera zinthu zikakhala momwazika kapena mong’ondoka. mae.: ng’ondo. itabuka ndewu mumsikamo malonda ambiri anatsakamuka ndipo anangoti balala ponseponse. balalika /tttk/ Ku-, mne. khala momwazika monga chimanga chikatayika. consider: choka pamalo kupita mbali zosiyanasiyana malinga ndi komwe aliyense wachokera. msonkhano utatha anthu onse anabalalika kupita kwawo. balamanthu mve. umo amaonekera munthu kapena chinthu chikatulukira kapena kuonekera poyera mwadzidzidzi. mae.: buchi, tulukiru. alenje anayamba kuthawa mkango utangoti balamanthu. balang’ombe dzi. Li-Ma- (zambi. mabalang’ombe) mavu akuluakulu akuda. mae mphang’ombe, chiphang’ombe, bavunyondo, chidazi. nkhope yake inatupa atalumidwa ndi mavu abalang’ombe. balani (Nge) /kt/ dzi. Li-Ma- (zambi. mabalani) nyumba yotchisiramo fodya. fodya wawo anawonongeka ndi mvula chifukwa balani yomwe amatchisiramo inali yothonya. balasuku (Pwi) dzi. Li-Ma- (zambi. mabalasuku) chidutswa chagalasi losweka. galasilo litaswanyika anasesa mabalasuku onse kuopa kuti anthu angawaponde ndi kubaidwa. balaula dzi. Mu- A- (zambi. abalaula) kachilombo kamtundu wagulugufe kokhala ndi mapiko anayi akuluakulu oyerera kapena amawangamawanga. mae.: pherupheru, chiphepheru. ndi kovuta kusiyanitsa gulugufe ndi balawula popeza tizilombo tiwiriti timafanana kwambiri. balawu dzi. Mu-A- (zambi. abalawu) nkhumba yaikulu yaimuna. popeza kuti anali ndi nkhumba zazikazi zokhazokha anapita kwa achimtengo kukabwereka balawu kuti nkhumba zawozo zikhale ndi bere. balaza (Swa) /tkt/ dzi. Li-Ma- (zambi. mabalaza) chipinda chochezeramo. kunekwi.: balanda. timakonda kucheza pa balaza ya nyumba yathu tsiku lililonse pambuyo pachakudya cha madzulo. bale (Nge) /kt/ dzi. Mu-A- (zambi. bale) mtundu wa fodya wamasamba ataliatali yemwe amamuwumitsa ndi dzuwa. chaka chamawa ndidzalima fodya wa bale kuti ndidzapeze ndalama zambiri. bama Ku-, mne. kumba pansi polimba ndi khasu kapena piki. kunekwi.: bamantha. mae.: bamanthula. khasu linabuntha pobama dzenje lotayamo zinyatsi. bambala dzi. Li-Ma- (zambi. mabambala) mpanda wozungulira khola la nkhumba kuti zisamatuluke. mae.: gwekwe. anamanga bambala la mitengo ya malaina pofuna kuti nkhumba zawo zisamatuluke. bambi /tk/ dzi. Li-Ma- (zambi. mabambi) mbali yaifupi ya chinthu monga nsalu. kunekwi.: bwambi. mae.: lifupi. nsalu yomwe anagula inali yamamita asanu mu litali ndi mamita awiri mu bambi. bambo dzi. Mu-A- (zambi. abambo) 1 kholo lalimuna. bambo wanga amagwira ntchito ku Lilongwe. 2 mwamuna aliyense wamkulu bambo akupita apowo akuyenda ngati aledzera. 3 wansembe wamipingo ina monga Katolika ndi Angilikani. akulu ampingo anapita kutchalitchi kukawadziwitsa bambo za kumwalira kwa mmodzi wa akhirisitu. bampala (Nge) /kt/ dzi. I-Zi-/ Li-Ma- (zambi. bampala/mabampala) chitsulo cha galimoto chokhala mopingasa kutsogolo kapena kumbuyo kwake chotchinjiriza galimoto ku zinthu zomwe ingagunde. galimoto ziwiri zitagundana, galimoto imodzi inaonongeka injini popeza bampala yake inali yosalimba. banda /tk/ dzi. I-Zi- (zambi. banda) mtundu wa nyerere zokulirapo zonga ndandu zomwe zili ndi miyendo italiitali. mwana anayamba kulira pamene banda zinamukwera pamwendo koma amake anamusasa mwa nsanga nyererezo. bandakula Ku-, mne. chotsa chotsekera cha pamphika, botolo kapena bokosi. mae. vundukula, funthukhula. ndiwozo zitabwata, anabandakula chivindikiriro kuti athire nchere. bandali /ttk/ dzi. Li-Ma- (zambi. mabandali) malo amene nyanja yalowa ku mtunda. mae.: nsolomondo, ndomo. alimi amabvala mbewu zosiyanasiyana mphepete mwa bandali makamaka madzi akasefukira. bandawe /kt/ dzi. Mu-A- (zambi. abandawe) mtundu wa chimanga chimene chili ndi chitsononkho chooneka ngati chadyedwa ndi chiswe. mae.: kachiswe. bungwe la Admarc laonjeza kuti chaka chino lidzagula kwa alimi chimanga cha mtundu wa bandawe chomwe chimatchedwanso kuti kachiswe. bande /kt/ dzi. Li-Ma- (zambi. mawande) 1 njira yowanda pa thengo. mae.: chikuwa. apolisi anapeza katundu yemwe mbala zinabisa m’tchire potsatira bande lomwe mbalayo inadzera pokabisa katunduyo. 2 mtundu wa udzu womera m’mbali mwa nyanja kapena mwa mtsinje. anamanga msasa wa udzu wa bande kuti azigonamo pamene anapita kukagula nsomba kwa asodzi kunyanja. bandeji (Nge) /kt/ dzi. Li-Ma- (zambi. mabandeji) kansalu komangira chilonda kapena malo opweteka. atanditsuka chilondacho ndi kuthirapo mankhwala, dokotala anandimanga bandegi pofuna kuti fumbi lisalowe pachilondacho. bandi (Nge) /kt/ dzi. I-Zi-/ Li-Ma- (zambi. bandi/mabandi) gulu la anthu oimba ndi zipangizo zoimbira moonga malipenga, zitoliro, gitala, ng’oma ndi zina. anthu anasangalala povina ku ukwati wa Mavuto ndi Chimwemwe chifukwa kunali bandi yodziwa kuyimba. bandira Ku- mne. 1 kwezera dothi pathumbira polima munthu akatha kupalira mbewu. mae.: chimbanda. kubandira mbewu ndi kofunika ngakhale kuti nthawi zina kumapangitsa kuuti mbewuzo zidyedwe ndi chiswe chifukwa cha dothi lokwezedwalo. 2 samba pa dziwe mwapholoso pochita nsambi. mnzanga anamira pa dziwe ilo chifukwa chosadziwa kubandira. bandu /tk/ dzi. Li-Ma- (zambi. mabandu) gawo limodzi la chinthu chathunthu likadulidwa monga dzungu. kunekwi.: chibandu. anandipatsa bandu la dzungu kuti ndidye koma sindinakhute. banduka Ku- mne. thamanga mofulumira kwambiri. dilayivala anachita ngozi pa gulaye chifukwa anali kubanduka kwambiri. bandula Ku-, mne. 1 waza chinthu cholimba monga nsungwi. mae.: walula. tengani thabwa lija kuseriko mubandule kuti tichite nkhuni. 2 consider: menya. amene akundinena ine ndimubandula mpaka atuluke magazi. banga dzi. Li-Ma- (zambi. mawanga) dontho la mtundu wina monga pa thupi la nyama kapena pa nsalu. mae.: thotho. chitenje chomwe amayi agula chili ndi banga la chikasu pakati. bango /kt/ dzi. Li-Ma- (zambi. mawango) chomera chonga udzu cha makwaule ataliatali osongoka chimene anthu amasoka mphasa ndipo chimamera m’mbali kapena mu mtsinje. bwato lomwe amapalasa litagadama, maliko anapulumuka osamira chifukwa anagwira bango m’mbali mwa mtsinjewo. bango /tk/ dzi. Li-Ma- (zambi. mango) chipatso chamtengo wamango chomwe chokhala ndi nthangala yaikulu yoyera m’kati mwake. mae.: lingo, yembe. mango akakhala aawisi amawawasa ndipo amakhala bwino kususira ndi mchere ndi tsabola. bangula /ttk/ Ku-, mne. 1 lira monga momwe umachitira mkango. mae.: uluma, luluma. alenje anayamba kuthawa pamene anamva kubangula kwa mkango. 2 fuula ndi mawu aakulu ndiponso amphamvu. pamene anapsa mtima, anayamba kubangula chifukwa cha ukali bangwe dzi. Mu- A- (zambi. abangwe) chipangizo choimbira chokhala ndi nsambo zisanu ndi ziwiri chomwe chimafana kwambiri ndi gitala. kunekwi.: pangwe. mae.: pango. nsambo zina za bangwe wake zinali zosakungika choncho sanali kumveka bwino. bani (Nge) /kt/ dzi. Li-Ma- (zambi. mabani) chakudya chofanana ndi sikono chopangidwa ndi ufa wa tirigu. iye anali ndi njala koma pamene anadya bani mkumwera madzi, mtima wake unatsika. banika /ttk/ Ku-, mne. leka kupuma kwa kanthawi pang’ono. mnyumbamo munali utsi wambiri kotero kuti anthu anayamba kubanika koma anayamba kupuma bwino atatsegula mazenera. banja /kt/ dzi. Li-Ma- (zambi. maanja) 1 mwamuna ndi mkazi wake. Mavuto ndi Chimwemwe anamanga banga chaka chatha. 2 maanja angapo otuluka nyumba m’banja limodzi. ?

See more

The list of books you might like

Most books are stored in the elastic cloud where traffic is expensive. For this reason, we have a limit on daily download.